Comsip Ithandiza kutukula chuma mdera la mfumu yayikulu chiwere

Comsip Ithandiza kutukula chuma mdera la mfumu yayikulu chiwere

Olemba: Wilson Allan Phiri
Mabanja a dera la Kasuza mdera la mfumu yayikulu chiwere m’boma la Dowa omwe amalandila ndalama za m’bwezela nthaka ndipo ali mumagulu akusunga komanso kuchulukitsa ndalama a Comsip ati magulu a Comsip akuwathandiza potukula chuma chawo komanso kukhala ndi kuthekera kwakukulu kobwezeletsa chilengedwe.
Malingana ndi Mayi Luka Anderson a mmudzi mwa nsenga, mumiyezi six yomwe akhala ali mu gulu losunga komanso kuchulukitsa ndalama la Comsip, akhwanitsa kugula makasu, mbeu komanso mbale.
“Ndakwanitsanso kuzindikila udindo wanga pa kusamalira chilengedwe kwinaku ndikutukula banja langa” anatero a Mayi Anderson.
Kumbari yake mlangizi wa chitukuko ku khonsolo ya Dowa a Sheila Masayiti ati mgwilizano omwe ulipo pakati pa khonsoloyi ndi bungwe la Comsip ukubweletsa chitukuko m’bomali.
Boma limapeleka thandizo la ndalama ku mabanja omwe ndiovutika akagwila ntchito za m’bwezela nthaka ngati malipiro ndipo bungwe la Comsip limasokhanitsa mwakufuna kwawo mabanjawa ndikuwaphunzitsa kufunika kosunga komanso kuchulukitsa ndalama zomwe amalandira.

Author